Ezekiel 29:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dziko la Ejipito lidzasanduka chipululu, lopanda anthu. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. “Zoona, iwe udati, ‘Nailo ndi wanga, ndidamlenga ndine.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi dziko la Ejipito lidzakhala lopasuka ndi labwinja; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, popeza anati, Mtsinjewo ndi wanga, ndinaulenga ndine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dziko la Igupto lidzasanduka lopanda anthu. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. “ ‘Popeza iwe unati, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga; ndinawupanga ndine,’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi dziko la Aigupto lidzakhala lopasuka ndi labwinja; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, popeza anati, Mtsinjewo ndi wanga, ndinaulenga ndine.