Ezekiel 3:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Mzimu wa Mulungu udandinyamula, ndipo kumbuyo kwanga ndidamva liwu lamphamvu ngati chivomezi chachikulu, lonena kuti, “Utamandike ulemerero wa Chauta kumene Iye amakhala!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mzimu unandinyamula, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau a mkokomo waukulu, ndi kuti, Wodala ulemerero wa Yehova m'malo mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Mzimu unandinyamula ndipo kumbuyo kwanga ndinamva liwu lamphamvu ngati chivomerezi chachikulu, lonena kuti, “Utamandike ulemerero wa Yehova kumene Iye amakhala!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mzimu unandinyamula, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau a mkokomo waukuru, ndi kuti, Wodala ulemerero wa Yehova m'malo mwace.