Ezekiel 3:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikauza munthu woipa kuti, ‘Munthu woipa iwe, udzafa,’ iwe nupanda kumchenjeza kuti aleke makhalidwe oipawo, kuti akhalebe ndi moyo, munthuyo adzafadi ali wochimwa, koma iweyo ndidzakuzenga mlandu chifukwa cha imfa yake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndikanena kwa woipa, Udzafa ndithu, koma iwe osamchenjeza, wosanena kumchenjeza woipayo aleke njira yake yoipa, kumsunga ndi moyo, woipa yemweyo adzafa mu mphulupulu yake; koma mwazi wake ndidzaufuna pa dzanja lako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndikawuza munthu woyipa kuti, ‘Iwe udzafa ndithu,’ koma iwe osamuchenjeza kapena kumuyankhula kuti aleke njira zake zoyipa ndi kuti akhale ndi moyo, munthu woyipayo adzafa mu uchimo wake, koma Ine ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndikanena kwa woipa, Udzafa ndithu, koma iwe osamcenjeza, wosanena kumcenjeza woipayo aleke njira yace yoipa, kumsunga ndi moyo, woipa yemweyo adzafa mu mphulupulu yace; koma mwazi wace ndidzaufuna pa dzanja lako.