Ezekiel 3:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ngati munthu wokhulupirira ayamba kuchita uchimo, Ine nkumuika m'zoopsa, ameneyo adzafa. Ngati iweyo sudamchenjeze, inde adzafa chifukwa cha kuchimwa kwakeko, ndipo kukhulupirika kwake sindidzakukumbukira, koma tsono mlandu wa imfa yake udzakhala pa iwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemonso akabwerera wolungama kuleka chilungamo chake, ndi kuchita chosalungama, ndipo ndikamuikira chomkhumudwitsa, adzafa; popeza sunamchenjeza, adzafa m'tchimo lake, ndi zolungama zake adazichita sizidzakumbukika; koma mwazi wake ndidzaufuna pa dzanja lako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ngati munthu wolungama asiya chilungamo chake ndi kuchita uchimo ndipo Ine nʼkumuyika mʼzoopsa, munthuyo adzafa ndithu. Popeza iwe sunamuchenjeze, adzafadi chifukwa cha tchimo ndipo chilungamo chake sichidzakumbukiridwa, koma ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemonso akabwerera wolungama kuleka cilungamo cace, ndi kucita cosalungama, ndipo ndikamuikira comkhumudwitsa, adzafa; popeza sunamcenjeza, adzafa m'cimo lace, ndi zolungama zace adazicita sizidzakumbukika; koma mwazi wace ndidzaufuna pa dzanja lako.