Ezekiel 3:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ukamchenjeza kuti asachimwe, iye nkulekadi kuchimwa, mosapeneka konse adzapulumutsa moyo wake, chifukwa chotsata chenjezo lako. Ndipo iwenso udzapulumutsa moyo wako.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ukamchenjeza wolungamayo, kuti asachimwe wolungamayo, ndipo sachimwa, adzakhala ndi moyo ndithu, popeza anachenjezedwa; ndipo iwe walanditsa moyo wako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati umuchenjeza munthu wolungama kuti asachimwe ndipo iye nʼkuleka kuchimwa adzakhala ndi moyo ndithu chifukwa anamvera chenjezo, ndipo iwe udzapulumutsa moyo wako.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ukamcenjeza wolungamayo, kuti asacimwe wolungamayo, ndipo sacimwa, adzakhala ndi moyo ndithu, popeza anacenjezedwa; ndipo iwe walanditsa moyo wako.