Ezekiel 3:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi ina ndidamva kuti mphamvu za Chauta zandiloŵa kwambiri, ndipo Iye adandiwuza kuti “Nyamuka, upite ku chigwa. Ndidzalankhula nawe kumeneko.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo dzanja la Yehova linandikhalira komweko, nati kwa ine, Nyamuka, tuluka kunka kuchidikha, ndipo pomwepo ndidzalankhula ndi iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi ina dzanja la Yehova linali pa ine ndipo anandiwuza kuti, “Nyamuka upite ku chigwa, kumeneko ndikayankhula nawe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo dzanja la Yehova linandikhalira komweko, nati kwa ine, Nyamuka, turuka kumka kucidikha, ndipo pomwepo ndidzalankhula ndi iwe.