Ezekiel 3:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho ndidanyamuka kupita ku chigwa. Kumeneko ndidaona ulemerero wa Chauta, monga momwe ndidaauwonera ku mtsinje wa Kebara. Pomwepo ndidadzigwetsa pansi chafufumimba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinauka ndi kutuluka kunka kuchidikha, ndipo taonani, ulemerero wa Yehova unaimako monga ulemerero uja ndinauona kumtsinje Kebara, ndipo ndinagwa nkhope pansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho ndinanyamuka kupita ku chigwa. Ndipo ndinaona ulemerero wa Yehova kumeneko, ngati ulemerero umene ndinaona mʼmbali mwa mtsinje wa Kebara ndipo ndinagwa pansi chafufumimba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinauka ndi kuturuka kumka kucidikha, ndipo taonani, ulemerero wa Yehova unaimako monga ulemerero uja ndinauona ku mtsinje Kebara, ndipo ndinagwa nkhope pansi.