Ezekiel 3:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pamene ndidzayambe kulankhula nawe, ndidzakupatsa mphamvu zolankhulira. Ndipo udzaŵauze kuti, ‘Zimene akunena Ambuye Chauta nzakutizakuti.’ Wofuna kumva, amve. Wosafuna kumva, akhale, popeza kuti anthuwo ngaupandu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pamene ndilankhula nawe ndidzatsegula pakamwa pako, nudzanena nao, Atero Yehova Mulungu. Wakumvera amvere, wosafuna kumvera akhale; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma pamene ndidzayankhula kwa iwe, ndidzatsekula pakamwa pako ndipo udzawawuza kuti, ‘Ambuye Yehova akuti zakutizakuti.’ Aliyense wofuna kumva amve ndipo wokana kumva, muleke akane; pakuti iwo ndi anthu opanduka.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pamene ndilankhula nawe ndidzatsegula pakamwa pako, nudzanena nao, Atero Yehova Mulungu. Wakumvera amvere, wasafuna kumvera akhale; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.