Ezekiel 3:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakulimbitsa kupambana thanthwe lina lililonse, kuti ukhale wolimba ngati mwala wa daimondi. Usachite nawo mantha anthu aupanduwo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndalimbitsa mutu wako woposa mwala wolimbitsitsa, usawaopa kapena kutenga nkhawa pamaso pao; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndidzakusandutsa wolimba ngati mwala wa dayimondi umene uposa thanthwe lina lililonse kulimba kwake. Usachite nawo mantha kapena kuopsedwa nawo. Paja anthuwa ndi awupandu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndalimbitsa mutu wako woposa mwala wolimbitsitsa, usawaopa kapena kutenga nkhawa pamaso pao; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.