Ezekiel 30:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo ndi anthu ake, mtundu wa anthu ankhalwe kwambiri aja, adzabwera kudzaononga dzikolo. Adzasolola malupanga ao kuti amenyane ndi Aejipito, ndipo dzikolo lidzadzaza ndi mitembo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iye ndi anthu ake pamodzi naye, woopsa amitundu, adzatengedwa aliononge dzikolo, nadzasololera Ejipito malupanga ao, ndi kudzaza dziko ndi ophedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye ndi gulu lake lankhondo, mtundu wa anthu ankhanza kwambiri aja adzabwera kudzawononga dzikolo. Adzasolola malupanga awo kulimbana ndi Igupto ndipo dziko lidzadzaza ndi mitembo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iye ndi anthu ace pamodzi naye, woopsa amitundu, adzatengedwa aliononge dzikolo, nadzasololera Aigupto malupanga ao, ndi kudzaza dziko ndi ophedwa.