Ezekiel 30:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzaumitsa mtsinje wa Nailo, ndipo Ejipito ndidzamgulitsa kwa anthu oipa. Dzikolo ndidzaliwononga, pamodzi ndi zonse zam'menemo, polipereka m'manja mwa anthu akudza. Ine Chauta ndatero.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzaphwetsa mitsinje, ndi kugulira dziko m'dzanja la anthu oipa, ndipo ndidzalisandutsa likhale dziko lopasuka, ndi zonse zili m'mwemo mwa dzanja la alendo; Ine Yehova ndachinena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzawumitsa mtsinje wa Nailo ndi kugulitsa dziko la Igupto kwa anthu oyipa. Ndidzagwiritsa ntchito anthu achilendo kuti ndiwononge dzikolo pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo. Ine Yehova ndayankhula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzaphwetsa mitsinje, ndi kugulira dziko m'dzanja la anthu oipa, ndipo ndidzalisandutsa likhale dziko lopasuka, ndi zonse ziri m'mwemo mwa dzanja la alendo; Ine Yehova ndacinena.