Ezekiel 30:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mzinda wa Peluziumu, linga lolimba la Ejipito, ndidzauthira mkwiyo wanga, ndipo ndidzaononga gulu lankhondo la ku Thebesi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzatsanulira ukali wanga pa Sini, polimbika penipeni pa Ejipito, ndi kulikha aunyinji a No.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzakhuthulira ukali wanga pa mzinda wa Peluziumu, linga lolimba la Igupto, ndi kuwononga gulu lankhondo la Thebesi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzatsanulira ukali wanga pa Sini, polimbika peni peni pa Aigupto, ndi kulikha aunyinji a No.