Ezekiel 30:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndikudana naye Farao, mfumu ya ku Ejipito. Ndidzamthyola manja onse, lamoyo ndi lothyokalo, ndipo lupanga lake lidzamtayika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona, Ine ndilimbana naye Farao mfumu ya Aejipito, ndidzathyola manja ake, lolimba ndi lothyokalo, ndi kutayitsa lupanga m'dzanja lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndikudana ndi Farao mfumu ya Igupto. Ndidzathyola manja ake onse; dzanja labwino pamodzi ndi lothyokalo, ndipo lupanga lidzagwa mʼmanja mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taona, Ine ndilimbana naye Parao mfumu ya Aigupto, ndidzatyola manja ace, lolimba ndi lotyokalo, ndi kutayitsa lupanga m'dzanja lace.