Ezekiel 30:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, ndipo m'manja mwake ndidzaikamo lupanga langa. Koma Farao ndidzamthyola manja, ndipo adzabuula ngati wolasidwa koopsa pamaso pa mfumu ya ku Babiloniyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, ndi kuika lupanga langa m'dzanja lake; koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuula pamaso pake mabuulo a munthu wopyozedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, ndipo mʼmanja mwake ndidzayikamo lupanga langa. Koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuwula ngati wolasidwa koopsa pamaso pa mfumu ya ku Babuloniyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babulo, ndi kuika lupanga langa m'dzanja lace; koma ndidzatyola manja a Parao, ndipo adzabuula pamaso pace mabuulo a munthu wopyozedwa.