Ezekiel 30:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndithu ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, koma manja a Farao adzafooka. Motero anthu adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzaika lupanga langa m'manja mwa mfumu ya ku Babiloni. Ndipo adzaligwiritsa ntchito pomenya nkhondo ndi dziko la Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, koma manja a Farao adzagwa; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova pakuika Ine lupanga langa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, nalitambasula iye pa dziko la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, koma manja a Farao adzafowoka. Motero anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzayika lupanga langa mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ndipo adzaligwiritsa ntchito pothira nkhondo dziko la Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babulo, koma manja a Parao adzagwa; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova pakuika Ine lupanga langa m'dzanja la mfumu ya ku Babulo, nalitambasula Iye pa dziko la Aigupto.