Ezekiel 30:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ku Ejipito kudzafika nkhondo, ndipo ku Etiopiya kudzagwa mavuto. Anthu ambiri adzaphedwa ku Ejipito, chuma chake chidzatengedwa, ndipo maziko ake adzagumuka.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi lupanga lidzadzera Ejipito, ndi m'Kusi mudzakhala kuwawa kwakukulu, pakugwa ophedwa m'Ejipito; ndipo adzachotsa aunyinji ake, ndi maziko ake adzagadamuka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lupanga lidzabwera kudzalimbana ndi Igupto ndipo mavuto adzafika pa Kusi. Pamene anthu ambiri adzaphedwa mu Igupto, chuma chake chidzatengedwa ndipo maziko ake adzagumuka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi lupanga lidzadzera Aigupto, ndi m'Kusi mudzakhala kuwawa kwakukuru, pakugwa ophedwa m'Aigupto; ndipo adzacotsa aunyinji ace, ndi maziko ace adzagadamuka,