Ezekiel 30:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nthaŵi imeneyo ikadzafika, amithenga adzapita mofulumira kuchokera kwa Ine kukaopsa Aetiopiya, iwowo osadziŵako kanthu. Ndipo adzada nkhaŵa pa tsiku limene Ejipito adzaonongedwa, chifukwa tsikulo lidzafika ndithu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku ilo mithenga idzatuluka pamaso panga m'zombo kuopsa Akusi osalabadira; ndipo kudzakhala kuwawa kwakukulu pakati pao, monga tsiku la Ejipito, pakuti taona, likudza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Nthawi imeneyo ikadzafika, amithenga adzapita mofulumira kuchokera kwa Ine kukaopseza Kusi, iwowo osadziwako kanthu. Ndipo adzada nkhawa pa tsiku limene Igupto adzawonongedwa, chifukwa tsikulo lidzafika ndithu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku ilo mithenga idzaturuka pamaso panga m'zombo kuopsa Akusi osalabadira; ndipo kudzakhala kuwawa kwakukuru pakati pao, monga tsiku la Aigupto, pakuti taona, likudza.