Ezekiel 31:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Alendo ankhalwe kwambiri pakati pa mitundu ya anthu adzaudula, ndipo adzangoutaya. Nthambi zake zidzagwera pa mapiri, ndiponso m'zigwa zonse. Nthambi zakezo zidzathyokera m'mitsinje yam'dzikomo. Motero anthu a mitundu yonse ya dziko lapansi amene ankasangalala mumthunzi mwake adzausiya nachoka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo alendo oopsawo a amitundu anaulikhatu, nausiya; nthawi zake zidagwa pamapiri ndi m'zigwa zonse, ndi nthambi zake zinathyokera ku timitsinje tonse ta m'dziko; ndi mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi inatsika kumthunzi wake, niusiya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ankhanza kwambiri amitundu ya anthu achilendo adzawudula ndi kuwusiya. Nthambi zake zidzagwera pa mapiri ndi mu zigwa zonse. Nthambi zake zidzathyokera mʼmitsinje ya mʼdzikomo. Motero mitundu yonse ya anthu a dziko lapansi amene ankasangalala mu mthunzi wake idzawusiya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo alendo oopsawo a amitundu anaulikhatu, nausiya; nthawi zace zidagwa pamapiri ndi m'zigwa zonse, ndi nthambi zace zinatyokera ku timitsinje tonse ta m'dziko; ndi mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi inatsika ku mthunzi wace, niusiya.