Ezekiel 31:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Zimene Ine Ambuye Chauta ndikunena ndi izi: Mkungudzawo utatsikira ku manda, ndidauza nyanja kuti iwulire maliro pa kuuphimba. Ndidaumitsa mitsinje yake, ndipo madzi ambiri adaphwa. Ndidachititsa mdima pa Lebanoni chifukwa cha mtengowo, ndipo mitengo yonse yam'dzikomo idauma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Ambuye Yehova, Tsiku lija anatsikira kumanda ndinachititsa maliro, ndinamphimbira nyanja, ndinachepsa mitsinje yake, ndi madzi aakulu analetseka; ndipo ndinamdetsera Lebanoni, ndi mitengo yonse ya kuthengo inafota chifukwa cha uwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa nthawi imene mkungudzawo unatsikira ku manda, ndinawuza nyanja kuti iwulire maliro pakuwuphimba. Ndinawumitsa mitsinje ndipo madzi ambiri anaphwa. Ndinabweretsa mdima pa Lebanoni chifukwa cha mtengowo ndipo mitengo yonse ya mʼdzikomo inawuma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Ambuye Yehova, Tsiku lija anatsikira kumanda ndinacititsa maliro, ndinamphimbira nyanja, ndinacepsa mitsinje yace, ndi madzi akuru analetseka; ndipo ndinamdetsera Lebano, ndi mitengo yonse ya kuthengo inafota cifukwa ca uwo.