Ezekiel 31:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mitundu ya anthu idagwedezeka pakumva mkokomo wa kugwa kwake, pamene ndidautsitsira ku manda pamodzi ndi amene adafa. Pamenepo ku dziko la akufa mitengo yonse ya ku Edeni, ndi yonse yokongola ya ku Lebanoni yothiriridwa bwino, idasangalatsidwa chifukwa cha zimenezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinagwedeza amitundu ndi phokoso la kugwa kwake, muja ndinagwetsera kumanda, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda; ndi mitengo yonse ya ku Edeni yosankhika, ndi yokometsetsa ya ku Lebanoni, yonse yakumwa madzi, inasangalala munsi mwake mwa dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mitundu ya anthu inagwedezeka pakumva mkokomo wa kugwa kwake, pamene ndinawutsitsira ku manda pamodzi ndi iwo amene anafa. Pamenepo ku dziko la akufa mitengo yonse ya ku Edeni pamodzi ndi ya ku Lebanoni yosankhidwa bwino inasangalatsidwa chifukwa cha zimenezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndirtagwedeza amitundu ndi phokoso la kugwa kwace, muja ndinamgwetsera kumanda, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda; ndi mitengo yonse ya ku Edene yosankhika, ndi yokometsetsa ya ku Lebano, yonse yakumwa madzi, inasangalala munsi mwace mwa dziko lapansi.