Ezekiel 31:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pakati pa mitengo ya ku Edeni, kodi unalipo ndi umodzi womwe wolingana nawe pa ulemerero ndi pa ukulu? Komabe iwenso udzatsikira ku dziko la akufa, pamodzi ndi mitengo ina yonse ya ku Edeni. Udzagona pamodzi ndi amene adaphedwa ku nkhondo, m'gulu la anthu osaumbalidwa! Mtengowo ndi mfumu ya ku Ejipito pamodzi ndi anthu ake. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo ufanana ndi yani m'ulemerero ndi ukulu pakati pa mitengo ya Edeni? Koma udzatsitsidwa pamodzi ndi mitengo ya Edeni munsi mwake mwa dziko lapansi, udzagona pakati pa osadulidwa, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga. Uwu ndi Farao ndi aunyinji ake onse, ati Ambuye Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ndi mitengo iti ya mu Edeni imene ingafanane ndi kukongola kwako ndi ulemerero wako? Komabe iwenso, udzatsikira ku dziko la anthu akufa pamodzi ndi mitengo ya mu Edeni. Udzagona pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, anthu amene anaphedwa pa nkhondo. “ ‘Mtengowo ndi Farao ndi gulu lake lankhondo, akutero Ambuye Yehova.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo ufanana ndi yani m'ulemerero ndi ukulu pakati pa mitengo ya Edene? koma udzatsitsidwa pamodzi ndi mitengo ya Edene munsi mwace mwa dziko lapansi, udzagona pakati pa osaditiidwa, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga. Uwu ndi Farao ndi aunyinji ace onse, ati Ambuye Yehova.