Ezekiel 31:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndithu ndidzakufanizirani ndi mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni, wa nthambi zabwino zochititsa mthunzi m'nkhalango, nthambi zosomphoka, zofika mpaka ku mitambo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona, Asiriya anali mkungudza wa ku Lebanoni ndi nthambi zokoma zovalira, wautali msinkhu, kunsonga kwake ndi kumitambo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani, ndidzakufanizirani ndi mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni, wa nthambi zokongola zochititsa mthunzi mʼnkhalango. Unali wautali, msonga zake zooneka pamwamba pa nkhalango.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona, Asuri anali mkungudza wa ku Lebano ndi nthambi zokoma zobvalira, wautali msinkhu, kunsonga kwace ndi kumitambo.