Ezekiel 31:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mtengo uwu udatalika kwambiri kupambana mtengo wina uliwonse. Nthambi zake zidachuluka ndi kutalika kwambiri, popeza kuti mizu yake inkalandira madzi ambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake msinkhu wake unaposa mitengo yonse ya kuthengo, ndi nthambi zake zinachuluka, ndi nthawi zake zinatalika, chifukwa cha madzi ambiri pophuka uwu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho unatalika kwambiri kupambana mitengo yonse ya mʼmunda. Nthambi zake zinachuluka ndi kutalika kwambiri, chifukwa inkalandira madzi ambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace msinkhu wace unaposa mitengo yonse ya kuthengo, ndi nthambi zace zinacuruka, ndi nthawi zace zinatalika, Cifukwa ca madzi ambiri pophuka uwu.