Ezekiel 31:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mbalame zamumlengalenga zinkamanga zisa zake m'nthambi za mtengowo. Nyama zonse zakuthengo zinkaswanirana m'munsi mwa nthambizo. Mitundu yonse yotchuka ya anthu inkakhala mumthunzi mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mbalame zonse za m'mlengalenga zinamanga zisa zao pa nthambi zake, ndi pansi pa nthawi zake zinaswana nyama zonse za kuthengo, ndi pa mthunzi wake inakhala mitundu yonse yaikulu ya anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mbalame zonse zamlengalenga zinkamanga zisa zake mʼnthambi za mtengowo. Nyama zakuthengo zonse zinkaswanirana mʼmunsi mwa nthambi zake. Mitundu yotchuka ya anthu inkakhala mu mthunzi wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mbalame zonse za m'mlengalenga zinamanga zisa zao pa nthambi zace, ndi pansi pa nthawi zace zinaswana nyama zonse za kuthengo, ndi pa mthunzi wace inakhala mitundu yonse yaikuru ya anthu.