Ezekiel 31:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'munda wa Mulungu munalibe mkungudza wofanafana ndi umenewo. Munalibe mtengo wa paini wa nthambi zofanafana ndi zake. Munalibenso mkuyu umene unali ndi nthambi zotere. M'munda wa Mulungu munalibe mtengo wina wofanafana ndi umenewu kukongola kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mikungudza ya m'munda wa Mulungu siinathe kuubisa, milombwa siinanga nthambi zake, mifula siinanga nthawi zake; m'munda wa Mulungu munalibe mtengo wofanana nao kukoma kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmunda wa Mulungu munalibe mkungudza wofanana nawo, kapena mitengo ya payini ya nthambi zofanafana ndi nthambi zake. Munalibenso mtengo wa mkuyu nthambi zofanafana ndi zake. Mʼmunda wa Mulungu munalibe mtengo wina uliwonse wofanana ndi iwo kukongola kwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mikungudza ya m'munda wa Mulungu siinathe kuubisa, milombwasimanga nthambi zace, mifula siinanga nthawi zace; m'munda wa Mulungu munalibe mtengo wofanana nao kukoma kwace.