Ezekiel 32:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzadabwitsa anthu ambiri ndi zimene zidzakugwere. Mafumu ao adzanjenjemera pokumbukira iwe, nditaŵaonetsa lupanga langa. Pa tsiku la kugwa kwako, aliyense adzadera nkhaŵa moyo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzasumwitsa nawe mitundu yambiri ya anthu, ndi mafumu ao adzachita malunga chifukwa cha iwe, pakung'animitsa Ine lupanga langa pamaso pao; ndipo adzanjenjemera mphindi zonse, yense chifukwa cha moyo wake tsiku lakugwa iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndidzachititsa kuti anthu a mitundu yambiri adabwe nawe, ndipo mafumu awo adzanjenjemera ndi mantha aakulu chifukwa cha iwe pamene ndidzaonetsa lupanga langa pamaso pawo. Pa nthawi ya kugwa kwako, aliyense wa iwo adzanjenjemera moyo wake wonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzasumwitsa nawe mitundu yambiri ya anthu, ndi mafumu ao adzacita malunga cifukwa ca iwe, pakung'animitsa Ine lupanga langa pamaso pao; ndipo adzanjenjemera mphindi zonse, yense cifukwa ca moyo wace tsiku lakugwa Iwe,