Ezekiel 32:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzagwetsa gulu lako lonse lankhondo ndi malupanga a asilikali oopsa kwambiri kupambana a mitundu ina yonse. “Adzathetsa kunyada kwa Ejipito, ndipo gulu lake lonse lankhondo lidzaonongeka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzagwetsa aunyinji ako ndi malupanga a eni mphamvu, ndiwo onse oopsetsa a amitundu; ndipo adzaipsa kudzikuza kwa Ejipito, ndi aunyinji ake onse adzaonongeka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzachititsa gulu lako lankhondo kuti ligwe ndi lupanga la anthu amphamvu, anthu ankhanza kwambiri pakati pa mitundu yonse ya anthu. Adzathetsa kunyada kwa Igupto, ndipo gulu lake lonse la nkhondo lidzagonjetsedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzagwetsa aunyinji ako ndi malupanga a eni mphamvu, ndiwo onse oopsetsa a amitundu; ndipo adzaipsa kudzikuza kwa Aigupto, ndi aunyinji ace onse adzaonongeka.