Ezekiel 32:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzaononga ziŵeto zao zonse zokhala pambali pa madzi am'dzikomo. Kumadziko sikudzaonekanso phazi la munthu, ndipo phazi la nyama silidzavonongeranso madzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzaononganso nyama zake zonse za kumadzi ambiri; ndi phazi la munthu silidzavundulira, ndi ziboda za nyama zosawavundulira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzawononga ziweto zake zonse zokhala mʼmbali mwa madzi ambiri. Ku madziko sikudzaonekanso phazi la munthu kapena kudetsedwa ndi phazi la ziweto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzaononganso nyama zace zonse za ku madzi ambiri; ndi phazi la munthu silidzabvundulira, ndi ziboda za nyama zosawabvundulira.