Ezekiel 32:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ejipito nditamsandutsa bwinja, ndipo dziko lonse nditaliwononga, nditapha onse okhala kumeneko, adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakusanduliza Ine dziko la Ejipito likhale lopasuka ndi labwinja, dziko losowa zodzaza zake, pakukantha Ine onse okhala m'mwemo, pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndikadzasandutsa dziko la Igupto kukhala bwinja; ndikadzawononga dziko lonse ndi kukantha onse okhala kumeneko, adzadziwa kuti ndine Yehova.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakusanduliza Ine dziko la Aigupto likhale lopasuka ndi labwinja, dziko losowa zodzaza zace, pakukantha Ine onse okhala m'mwemo, pamenepo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.