Ezekiel 32:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Iwe mwana wa munthu, imbira Farao, mfumu ya ku Ejipito, nyimbo yamaliro. Umuuze uthenga uwu wakuti: “Iwe umadziyesa mkango pakati pa mitundu ya anthu, koma uli ngati ng'ona. Umakhuvula m'mitsinje yako. Umavonongera madzi ndi mapazi ako, ndi kudetserera mitsinje.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wobadwa ndi munthu iwe, takwezera Farao mfumu ya Aejipito nyimbo yamaliro; uziti naye, Unafanana nao msona wa mkango wa amitundu, unanga ng'ona ya m'nyanja, unabuka m'mitsinje mwako, nuvundulira madzi ndi mapazi ako, ndi kudetsa mitsinje yao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iwe mwana wa munthu imba nyimbo ya maliro a Farao mfumu ya Igupto ndipo uyiwuze kuti, “Iwe umadziyesa ngati mkango pakati pa mitundu ya anthu. Koma iwe uli ngati ngʼona mʼnyanja. Umakhuvula mʼmitsinje yako, kuvundula madzi ndi mapazi ako ndi kudetsa madzi mʼmitsinje.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wobadwa ndi munthu iwe, takwezera Farao mfumu ya Aigupto nyimbo yamaliro; uziti naye, Unafanana nao msona wa mkango wa amitundu, unanga ng'ona ya m'nyanja, unabuka m'mitsinje mwako, nubvundulira madzi ndi mapazi ako, ndi kudetsa mitsinje yao.