Ezekiel 32:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Manda ao ali m'malo ozama kwambiri m'dziko la anthu akufa, ndipo manda ao adazungulira manda ake. Iwowo kale ankaopsa m'dziko la anthu amoyo, koma tsopano onsewo adafa, adaphedwa pa nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
manda ao aikidwa ku malekezero a dzenje, ndi gulu lake lizinga manda ake; ophedwa onsewo adagwa ndi lupanga, amene anopsetsa m'dziko la amoyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Manda awo ali kumalo ozama a dzenje, ndipo ankhondo ake azungulira manda ake. Onse amene anaopseza dziko la anthu amoyo aphedwa, agwa ndi lupanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
manda ao aikidwa ku malekezero a dzenje, ndi gulu lace lizinga manda ace; ophedwa onsewo adagwa ndi lupanga, amene anaopsetsa m'dziko la amoyo.