Ezekiel 32:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Komweko kulinso Elamu ndipo ankhondo ake onse ali m'manda omzungulira. Onsewo adaphedwa pa nkhondo. Anthuwo adatsikira ku manda ali osaumbalidwa. Iwowo kale ankaopsa m'dziko la anthu amoyo. Tsopano akuchita manyazi, pamodzi ndi amene ali m'manda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Elamu ali komwe ndi gulu lake lonse lozinga manda ake; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga; amene anatsikira osadulidwa kunsi kwake kwa dziko, amene anaopsetsa m'dziko la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Elamu ali komweko ndipo ankhondo ake ali mʼmanda omuzungulira. Onsewa anaphedwa pa nkhondo, natsikira ku manda ali osachita mdulidwe. Iwowa kale ankaopseza anthu pa dziko lapansi. Tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali mʼmanda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Elamu ali komwe ndi gulu lace lonse lozinga manda ace; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga; amene anatsikira osadulidwa kunsi kwace kwa dziko, amene anaopsetsa m'dziko la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.