Ezekiel 32:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Elamuyo amupangira malo ogonapo pakati pa anthu ophedwa, pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo, loikidwa momzungulira. Onsewo ndi osaumbalidwa, ophedwa pa nkhondo. Zoonadi, anthu amene kale ankaopsa m'dziko la anthu amoyo, tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali m'dziko la anthu akufa. Aikidwa pakati pa anthu ophedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakati pa ophedwa anamuikira kama, iye ndi aunyinji ake onse, manda ake amzinga, onsewo osadulidwa, ophedwa ndi lupanga, pakuti anaopsetsa la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje, aikidwa pakati pa ophedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amukonzera pogona pakati pa anthu ophedwa, pamodzi ndi gulu lake lonse la nkhondo litazungulira manda ake. Onsewo ndi anthu osachita mdulidwe ophedwa ndi lupanga. Paja anthuwa ankaopsa mʼdziko la anthu a moyo. Koma tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali mʼmanda. Iwo ayikidwa pakati pa anthu ophedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakati pa ophedwa anamuikira kama, iye ndi aunyinji ace onse, manda ace amzinga, onsewo osadulidwa, ophedwa ndi lupanga, pakuti anaopsetsa m'dziko la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje, aikidwa pakati pa ophedwa,