Ezekiel 32:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Komwekonso kuli Meseki ndi Tubala. Ankhondo ao onse ali m'manda oŵazungulira. Anthuwo ndi osaumbalidwa, ndipo adaphedwa pa nkhondo. Iwowo kale ankaopsa m'dziko la anthu amoyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Meseki, Tubala, ndi aunyinji ake onse ali komweko, manda ake amzinga; onsewo osadulidwa, ophedwa ndi lupanga; pakuti anaopsetsa m'dziko la amoyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mesaki ndi Tubala ali komweko, pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo litazungulira manda awo. Onsewo ndi anthu osachita mdulidwe, ophedwa ndi lupanga. Paja ankaopsa mʼdziko la anthu amoyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Meseke, Tubala, ndi aunyinji ace onse ali komweko, manda ace amzinga; onsewo osadulidwa, ophedwa ndi lupanga; pakuti anaopsetsa m'dziko la amoyo.