Ezekiel 32:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sadaikidwe mwaulemu ngati ankhondo amphamvu amakedzana, amene adatsikira ku dziko la anthu akufa ndi zida zao zomwe zankhondo. Malupanga ao adaŵaika ku mitu yao, ndipo zishango zao adaphimbira mafupa ao. Kale anthu amphamvu ameneŵa ankaopsa m'dziko la anthu amoyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma sagona pamodzi ndi amphamvu osadulidwa adagwawo amene anatsikira kumanda ndi zida zao za nkhondo, amene anawatsamiritsa malupanga ao; ndi mphulupulu zao zili pa mafupa ao; pakuti anaopsetsa amphamvu m'dziko la amoyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo sanayikidwe mwaulemu ngati ankhondo amphamvu amakedzana, amene anatsikira ku dziko la anthu akufa ndi zida zawo zomwe za nkhondo. Malupanga awo anawayika ku mitu yawo, ndipo zishango zawo anaphimba mafupa awo. Kale anthu amphamvu amenewa ankaopsa dziko la anthu amoyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma sagona pamodzi ndi amphamvu osadulidwa adagwawo amene anatsikira kumanda ndi zida zao za nkhondo, amene anawatsamiritsa malupanga ao; ndi mphulupulu zao ziri pa mafupa ao; pakuti anaopsetsa amphamvu m'dziko la amoyo.