Ezekiel 32:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komweko kuli Edomu pamodzi ndi mafumu ake ndi akalonga ake onse. Ngakhale anali amphamvu, komabe adaikidwa m'manda. Akugona pamodzi ndi anthu osaumbalidwa, pamodzi ndi onse amene adatsikira ku dziko la anthu akufa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Edomu ali komwe, mafumu ake ndi akalonga ake onse, amene anaikidwa mu mphamvu yao, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga; agona pamodzi ndi osadulidwa, ndi iwo akutsikira kudzenje.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Edomu ali kumeneko pamodzi ndi mafumu ake ndi akalonga ake onse. Ngakhale anali amphamvu, koma anayikidwa. Ayikidwa pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, pamodzi ndi iwo amene akutsikira ku dzenje.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Edomu ali komwe, mafumu ace ndi akalonga ace onse, amene anaikidwa mu mphamvu yao, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga; agona pamodzi ndi osadulidwa, ndi iwo akutsikira kudzenje.