Ezekiel 32:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Komweko kulinso akalonga onse akumpoto, pamodzi ndi anthu onse a ku Sidoni, amene adatsikira ku dziko la anthu akufa mwamanyazi, pamodzi ndi ophedwa, ngakhale anali oopsa ndi mphamvu zao. Akugona osaumbalidwa pamodzi ndi ophedwa pa nkhondo. Kumeneko akuchita manyazi pamodzi ndi onse amene adatsikira kale ku dziko la anthu akufa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akalonga a kumpoto ali komwe onsewo, ndi Asidoni onse, amene anatsikira pamodzi ndi ophedwa, nachita manyazi chifukwa cha kuopsetsa anachititsaku ndi mphamvu yao, nagona osadulidwa pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga, nasenza manyazi ao pamodzi ndi iwo otsikira kudzenje.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Akalonga onse akumpoto pamodzi ndi anthu onse a ku Sidoni ali kumeneko. Anatsikira ku dziko la anthu akufa mwamanyazi ngakhale anali owopsa ndi mphamvu zawo. Iwo akugona osachita mdulidwe pamodzi ndi amene anaphedwa ndi lupanga ndipo akuchita manyazi pamodzi ndi iwo amene anatsikira kale ku manda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akalonga a kumpoto ali komwe onsewo, ndi Azidoni onse, amene anatsikira pamodzi ndi ophedwa, nacita manyazi cifukwa ca kuopsetsa anacititsaku ndi mphamvu yao, nagona osadulidwa pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga, nasenza manyazi ao pamodzi ndi iwo otsikira kudzenje.