Ezekiel 32:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakuponya ku mtunda ndi kukutaya pansi. Ndidzabweretsa mbalame zamumlengalenga kuti zidzatere pa iwe, ndiponso zilombo za m'dziko lonse kuti zidzakudye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzakusiya pamtunda, ndidzakuponya kuthengo koyera, ndi kuteretsa pa iwe mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi kukhutitsa zilombo za dziko lonse lapansi ndi iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzakuponya ku mtunda ndi kukutayira pansi. Ndidzabweretsa mbalame zamumlengalenga kuti zidzatere pa iwe, ndipo zirombo zonse za dziko lapansi zidzakudya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzakusiya pamtunda, ndidzakuponya kuthengo koyera, ndi kuteretsa pa iwe mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi kukhutitsa zirombe za dziko lonse lapansi ndi iwe.