Ezekiel 33:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndithudi, pali Ine ndemwe, sindikondwa ndikaona munthu woipa alikufa. Ndikadakonda kuti aleke kuchimwako kuti akhale ndi moyo. Inu Aisraele, muferanji? Tembenukani, lekani zoipa zimene mukuchita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Uziti nao, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu nyumba ya Israele?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uwawuze kuti, Ine Ambuye Yehova ndikuti: “Pali Ine wamoyo, sindikondwera ndi imfa ya munthu woyipa. Ndimakondwera ndikamaona munthu woyipa akuleka zoyipa zake kuti akhale ndi moyo. Tembenukani! Tembenukani, siyani makhalidwe anu oyipa! Muferanji, Inu Aisraeli?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Uziti nao, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yace, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu nyumba ya Israyeli?