Ezekiel 33:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono iwe mwana wa munthu, uza anthu ako kuti, Pamene munthu wochita chifuniro cha Mulungu achimwa, zabwino zimene adaachita sizidzampulumutsa. Woipa akaleka kuchimwa, sadzalangidwa. Ndipo munthu wochita chifuniro cha Mulungu akayamba kuchimwa, sadzatha kukhala ndi moyo chifukwa cha ntchito zake zabwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, unene ndi ana a anthu a mtundu wako, Cholungama cha wolungama sichidzamlanditsa tsiku la kulakwa kwake, ndi kunena za choipa cha woipa, sadzagwa nacho tsiku lakubwerera iye kuleka choipa chake; ndi munthu wolungama sadzakhoza kukhala ndi moyo ndi chilungamo chake tsiku lakuchimwa iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono iwe mwana wa munthu, awuze anthu a mtundu wako kuti, ‘Ngati munthu wolungama achimwa, ndiye kuti ntchito zake zabwino zija sizidzamupulutsa. Koma wochimwa akaleka ntchito zake zoyipazo, sadzalangidwa konse. Ndithu ngati munthu wolungama ayamba kuchimwa sadzatha kukhala ndi moyo chifukwa cha ntchito zake zabwino zija.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, unene ndi ana a anthu amtundu wako, Colungama ca wolungama sicidzamlanditsa tsiku la kulakwa kwace, ndi kunena za coipa ca woipa, sadzagwa naco tsiku lakubwerera iye kuleka coipa cace; ndi munthu wolungama sadzakhoza kukhala ndi moyo ndi cilungamo cace tsiku lakucimwa iye.