Ezekiel 33:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale ndiwuze munthu wochita chifuniro cha Mulungu kuti adzakhala ndi moyo, ngati iye agonera pa zabwino zimene adaachita kale, nayamba kuchimwa, zabwino zake zonse zimene adaachitazo zidzaiŵalika. Adzafera zochimwa zakezo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndikanena kwa wolungama kuti adzakhala ndi moyo ndithu, akatama chilungamo chake, akachita chosalungama, sizikumbukika zolungama zake zilizonse; koma m'chosalungama chake anachichita momwemo adzafa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati ndiwuza munthu wolungama kuti adzafa ndithu, koma iyeyo nʼkumadalira ntchito zake zabwino zimene anachita kale ndi kuyamba kuchimwa, ndiye kuti ntchito zake zabwinozo zidzayiwalika. Iye adzafa chifukwa cha machimo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndikanena kwa wolungama kuti adzakhala ndi moyo ndithu, akatama cilungamo cace, akacita cosalungama, sizikumbukika zolungama zace ziri zonse; koma m'cosalungama cace anacicita momwemo adzafa.