Ezekiel 33:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
monga kubweza chigwiriro chimene adatenga chifukwa cha ngongole, kubweza zimene adaba, kusiya zochimwa ndi kumasunga malamulo opatsa moyo, ndithu sadzafa, adzakhala ndi moyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
woipayo akabweza chikole, nakabweza icho anachilanda mwachifwamba, nakayenda m'malemba a moyo wosachita chosalungama, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
monga kubweza chimene anatenga ngati chikole cha ngongole, kubweza chimene anaba, kutsatira malamulo omwe amapereka moyo ndi kuleka kuchita zoyipa, iye adzakhala ndithu ndi moyo; sadzafa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
woipayo akabweza cikole, nakabweza ico anacilanda mwacifwamba, nakayenda m'malemba a moyo wosacita cosalungama, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.