Ezekiel 33:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthunso woipa, akaleka kuchimwa, namachita zolungama ndi zabwino, adzapulumutsa moyo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo woipa akabwerera kuleka choipa chake, nakachita choyenera ndi cholungama, adzakhala ndi moyo nazo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngati munthu woyipa atembenuka ndi kuleka ntchito zake zoyipa ndi kuyamba kuchita zolungama ndi zoyenera, iye adzakhala ndi moyo pochita zimenezo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo woipa akabwerera kuleka coipa cace, nakacita coyenera ndi colungama, adzakhala ndi moyo nazo.