Ezekiel 33:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Iwe mwana wa munthu, uza anthu a mtundu wako zimene zimachitika ndikatumiza nkhondo m'dziko. Suja anthu am'dzikomo amasankha mmodzi pakati pao kuti akhale mlonda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wobadwa ndi munthu iwe, Nena ndi ana a anthu a mtundu wako, uziti nao, Ndikafikitsira dziko lililonse lupanga, nakatenga eni dziko munthu wa pakati pao, nakamuika awadikirire,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iwe mwana wa munthu awuze anthu a mtundu wako kuti, ‘Paja zimati ndikatumiza nkhondo mʼdziko anthu a mʼdzikomo amasankha munthu mmodzi pakati pawo kuti akhale mlonda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wobadwa ndi munthu iwe, Nena ndi ana a anthu a mtundu wako, uziti nao, Ndikafikitsira dziko liri lonse lupanga, nakatenga eni dziko munthu wa pakati pao, nakamuika awadikirire,