Ezekiel 33:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku lachisanu la mwezi wakhumi, chaka cha khumi ndi chiŵiri cha ukapolo wathu, munthu amene adapulumuka ku Yerusalemu, adabwera kudzandiwuza kuti mzinda wagwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chiwiri cha undende wathu, mwezi wakhumi, tsiku lachisanu la mweziwo, anandidzera wina wopulumuka ku Yerusalemu, ndi kuti, Wakanthidwa mudzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku lachisanu la mwezi wakhumi, chaka chakhumi ndi chiwiri cha ukapolo wathu, munthu wina amene anapulumuka ku Yerusalemu anabwera kudzandiwuza kuti, “Mzinda wagwa!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali caka cakhumi ndi ciwiri ca undende wathu, mwezi wakhumi, tsiku lacisanu la mweziwo, anandidzera wina wopulumuka ku Yerusalemu, ndi kuti, Wakanthidwa mudzi.