Ezekiel 33:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Madzulo, iyeyo asanabwere, ndidaagwidwa ndi mphamvu za Chauta. Koma m'maŵa mwake, munthuyo atafika, Chauta adandibwezera mphamvu zolankhulira, ndipo sindinalinso bububu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma dzanja la Yehova linandikhalira madzulo, asanandifike wopulumukayo; ndipo ananditsegula pakamwa mpaka anandifika m'mawa, m'mwemo panatseguka pakamwa panga, wosakhalanso wosalankhula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono madzulo ake munthuyo asanafike, dzanja la Yehova linali pa ine. Koma mmawa mwake munthuyo atabwera Yehova anatsekula pakamwa panga, motero kuti sindinakhalenso wosayankhula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma dzanja la Yehova linandikhalira madzulo, asanandifike wopulumukayo; ndipo ananditsegula pakamwa mpaka anandifika m'mawa, m'mwemo panatseguka pakamwa panga, wosakhalanso wosalankhula.