Ezekiel 33:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Iwe mwana wa munthu, anthu amene akukhala m'mizinda yamabwinja ku dziko la Israele, akunena kuti, ‘Abrahamu anali munthu mmodzi yekha, ndipo adamupatsa dziko lonse. Koma ife tilipo ambiri, motero tsopano dzikolo ndi lathu.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wobadwa ndi munthu iwe, iwo okhala kumabwinja a dziko la Israele anena, ndi kuti, Abrahamu anali yekha, nakhala nalo dziko cholowa chake; koma ife ndife ambiri, dzikoli lipatsidwa kwa ife cholowa chathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iwe mwana wa munthu, anthu amene akukhala mʼmizinda ya mabwinja ya dziko la Israeli akunena kuti, ‘Abrahamu anali munthu mmodzi yekha, ndipo anamupatsa dziko lonse. Koma ife tilipo ambiri, motero tsono dzikolo ndi lathu.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wobadwa ndi munthu iwe, iwo okhala ku mabwinja a dziko la Israyeli anena, ndi kuti, Abrahamu anali yekha, nakhala nalo dziko colowa cace; koma ife ndife ambiri, dzikoli lipatsidwa kwa ife colowa cathu.