Ezekiel 33:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, ‘Mumadya nyama pamodzi ndi magazi omwe. Mumapembedza mafano, mumapha anthu. Kodi tsono dzikolo nkudzakhaladi lanu?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake unene nao, Atero Ambuye Yehova, Mumadyera kumodzi ndi mwazi, mumakwezera maso anu kumafano anu, ndi kukhetsa mwazi; ndipo kodi mudzakhala nalo dziko cholowa chanu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho iwe uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Inu mumadya nyama ili ndi magazi ake, ndipo mumapembedza mafano ndi kukhetsa magazi, kodi tsono inu nʼkulandira dzikoli?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace unene nao, Atero Ambuye Yehova, Mumadyera kumodzi ndi mwazi, mumakwezera maso anu ku mafano anu, ndi kukhetsa mwazi; ndipo kodi mudzakhala nalo dziko colowa canu?