Ezekiel 33:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uŵauze kuti, Ine Ambuye Chauta ndikuti, Pali ine ndemwe wamoyo, anthu amene adatsala m'mizinda yamabwinja, adzaphedwa ndi lupanga. Amene adatsala m'midzi, ndidzaŵapereka ku zilombo kuti ziŵadye. Amene adabisala m'mapiri ndi m'mapanga, adzafa ndi mliri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Uzitero nao, Atero Ambuye Yehova, Pali Ine, iwo okhala kumabwinja adzagwadi ndi lupanga, ndi iye ali kuthengo koyera ndidzampereka kwa zilombo, adyedwe nazo; ndi iwo okhala m'malinga ndi m'mapanga adzafa ndi mliri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Ndithu pali Ine wamoyo, anthu amene anatsala mʼmizinda ya mabwinja adzaphedwa ndi lupanga, amene ali ku midzi ndidzawapereka kuti adzadyedwe ndi zirombo zakuthengo, ndipo amene ali mʼmalinga ndi mʼmapanga adzafa ndi mliri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Uzitero nao, Atero Ambuye Yehova, Pali Ine, iwo okhala kumabwinja adzagwadi ndi lupanga, ndi iye ali kuthengo koyera ndidzampereka kwa zirombo, adyedwe nazo; ndi iwo okhala m'malinga ndi m'mapanga adzafa ndi mliri.