Ezekiel 33:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dzikolo ndidzalisandutsa tsala ndiponso chipululu. Mphamvu zimene ankanyada nazo zidzatheratu. Mapiri a ku Israele adzasanduka thengo, kotero kuti munthu sadzadutsako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzasanduliza dziko likhale lachipululu ndi lodabwitsa, ndi mphamvu yake yodzikuza idzatha, ndi mapiri a Israele adzakhala achipululu, osapitako munthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzalisandutsa chipululu dzikolo, ndipo mphamvu zake zimene amanyadira zidzatheratu, ndipo mapiri a Yerusalemu adzasanduka chipululu, kotero kuti palibe amene adzatha kudutsako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzasanduliza dziko likhale lacipululu ndi lodabwitsa, ndi mphamvu yace yodzikuza idzatha, ndi mapiri a Israyeli adzakhala acipululu, osapitako munthu.